1 Chronicles 2

Ana a Israeli

1Ana a Israeli anali awa:
Rubeni, Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, Zebuloni,
2Dani, Yosefe, Benjamini, Nafutali, Gadi ndi Aseri.

Yuda Mpaka pa Ana a Hezironi

Ana a Hezironi

3Ana a Yuda anali awa:
Eri, Onani ndi Sela. Ana atatu awa anabereka ndi mkazi wa Chikanaani, Batisuwa. Eri, mwana woyamba wa Yuda anali woyipa kwambiri pamaso pa Yehova, kotero Yehova anamupha.
4Mpongozi wake Tamara anamuberekera Perezi ndi Zera. Ana onse a Yuda analipo asanu.

5Ana a Perezi anali awa:
Hezironi ndi Hamuli.
6Ana a Zera anali awa:
Zimuri, Etani, Hemani, Kalikoli ndi Dara. Onse analipo asanu.
7Mwana wa Karimi anali
Akani, amene anabweretsa mavuto pakati pa Israeli pamene anatenga zinthu zoyenera kuwonongedwa.
8Mwana wa Etani anali
Azariya.
9Ana amene anabadwa kwa Hezironi anali:
Yerahimeeli, Ramu ndi Kelubai.

Kuchokera kwa Ramu Mwana wa Hezironi

10Ramu anabereka
Aminadabu ndipo Aminadabu anali abambo ake a Naasoni, mtsogoleri wa fuko la Yuda.
11Naasoni anabereka Salima, Salima anabereka Bowazi, 12Bowazi anabereka Obedi ndipo Obedi anabereka Yese.
13Yese anabereka
Eliabu mwana wake woyamba, wachiwiri Abinadabu, wachitatu Simea,
14wachinayi Netaneli, wachisanu Radai, 15wachisanu ndi chimodzi Ozemu ndi wachisanu ndi chiwiri Davide. 16Alongo awo anali Zeruya ndi Abigayeli. Ana atatu a Zeruya anali Abisai Yowabu ndi Asaheli. 17Abigayeli anali amayi ake a Amasa amene abambo ake anali Yeteri wa fuko la Ismaeli.

Kalebe Mwana wa Hezironi

18Kalebe mwana wa Hezironi anabereka ana mwa Azuba mkazi wake (ndi mwa Yerioti). Ana a mkaziyo anali awa: Yeseri, Sobabu ndi Aridoni. 19Azuba atamwalira, Kalebe anakwatira Efurata, amene anamuberekera Huri. 20Huri anabereka Uri ndipo Uri anabereka Bezaleli.
21Patapita nthawi, Hezironi anagona ndi mwana wamkazi wa Makiri abambo ake a Giliyadi (iye anamukwatira ali ndi zaka 60) ndipo anamuberekera Segubu. 22Segubu anabereka Yairi, amene anali ndi mizinda 23 ku Giliyadi. 23(Koma Gesuri ndi Aramu analanda Havoti Yairi komanso Kenati ndi madera ake onse ozungulira, mizinda makumi asanu ndi umodzi). Onsewa anali adzukulu, a Makiri abambo ake a Giliyadi.

24Atamwalira Hezironi ku Kalebe Efurata, Abiya mkazi wa Hezironi anamuberekera Asihuri abambo a Tekowa.

Yerahimeeli Mwana wa Hezironi

25Ana a Yerahimeeli, mwana woyamba wa Hezironi anali:
Ramu, mwana wake woyamba, Buna, Oreni, Ozemu ndi Ahiya.
26Yerahimeeli anali ndi mkazi wina amene dzina lake linali Atara, amene anali amayi a Onamu.
27Ana a Ramu, mwana woyamba wa Yerahimeeli, anali awa:
Maazi, Yamini ndi Ekeri.
28Ana a Onamu anali awa:
Shamai ndi Yada.
Ana a Shamai anali awa:
Nadabu ndi Abisuri.
29Mkazi wa Abisuri anali Abihaili, amene anamuberekera Ahibani ndi Molidi.
30Ana a Nadabu anali awa:
Seledi ndi Apaimu. Koma Seledi anamwalira wopanda ana.
31Ana a Apaimu anali awa:
Isi, amene anabereka Sesani.
Sesani anabereka Ahilai.
32Ana a Yada, mʼbale wa Samai, anali awa:
Yereri ndi Yonatani. Koma Yeteri anamwalira wopanda ana.
33Ana a Yonatani anali awa:
Peleti ndi Zaza.
Amenewa anali adzukulu a Yerahimeeli.
34Sesani sanabereke ana aamuna koma aakazi okhaokha.
Iye anali ndi wantchito wa ku Igupto, dzina lake Yariha.
35Sesani anapereka mwana wake wamkazi kwa Yariha wantchito wake kuti amukwatire ndipo anamuberekera Atayi.
36Atayi anali abambo ake a Natani,
Natani anali abambo ake a Zabadi,
37Zabadi anali abambo a Efilali,
Efilali anali abambo a Obedi,
38Obedi anali abambo a Yehu,
Yehu anali abambo a Azariya,
39Azariya anali abambo a Helezi,
Helezi anali abambo a Eleasa,
40Eleasa anali abambo ake a Sisimai,
Sisimai anali abambo a Salumu,
41Salumu anali abambo a Yekamiya,
Yekamiya anali abambo a Elisama.

Mabanja a Kalebe

42Ana a Kalebe mʼbale wa Yerahimeeli anali awa:
Mesa mwana wachisamba, anali abambo a Zifi, ndipo mwana wake Maresa anali abambo a Hebroni.
43Ana a Hebroni anali awa:
Kora, Tapuwa, Rekemu ndi Sema.
44Sema anali abambo ake Rahamu ndipo Rahamu anali abambo a Yorikeamu. Rekemu anali abambo a Samai. 45Mwana wa Samai anali Maoni, ndipo Maoni anali abambo a Beti Zuri.
46Efai, mzikazi wa Kalebe, anali amayi a Harani, Moza ndi Gazezi. Harani anali abambo a Gazezi.
47Ana a Yahidai anali awa:
Regemu, Yotamu, Gesani, Peleti, Efai ndi Saafi.
48Maaka mzikazi wa Kalebe anali mayi Seberi ndi Tirihana. 49Iye anaberekanso Saafi abambo a Madimena ndi Seva abambo a Makibena ndi Gibeya. Mwana wamkazi wa Kalebe anali Akisa. 50Izi zinali zidzukulu za Kalebe.

Ana a Huri mwana wachisamba wa Efurata anali awa:
Sobala abambo a Kiriati Yearimu,
51Salima abambo a Betelehemu ndi Harefu abambo ake a Beti-Gadera.
52Zidzukulu za Sobala abambo a Kiriati Yearimu zinali izi:
Harowe, theka la banja la Manahati,
53ndipo mabanja a Kiriati-Yeyarimu anali awa: Aitiri, Aputi, Asumati ndi Amisirai. Azorati ndi Aesitaoli anachokera kwa amenewa.
54Zidzukulu za Salima zinali izi:
Betelehemu, Anetofati, Atiroti-Beti-Yowabu, theka la banja la Manahati, Azori,
55ndiponso mabanja a alembi amene amakhala ku Yabesi: Atiroti, Asimeati ndiponso Asukati. Awa ndi Akeni amene anachokera kwa Hamati, kholo la Arekabu.
Copyright information for NyaCCL